Nduna yoona zamadzi ndi ukhondo, a Abida Mia, yadzudzula mchitidwe owononga ma pipe a amadzi komanso kuba zipangizo zothandizira kugawa madzi m’dziko muno.
A Mia amayankhula izi mumzinda wa Lilongwe pamene anatsogolera mwambo otsekulira paipi yamadzi aulere kwa anthu aku Area 28 imene a kampani ya Sungold Food Processing Limited apereka kuti ithandize anthu mderali kupewa matenda odza kamba komwa madzi osatetezeka.
Izi zikudza pomwenso kanema wina anaonetsa amayi ena akuswa mapayipi amadzi, zomwe ndunayi yati ndi mchitidwe odzikonda.
Mkulu wakampani ya Sungold Food Processing Limited, a Mahesh Ghedia, ati iyi ndi ntchito yomwe yangoyamba ndipo mabilu onse amadziwa idzilipira ndi kampaniyi.
Phungu wadera lapakati mumzinda wa Lilongwe, a Alfred Jiya, wayamikira ntchitoyi ndipo wati udindo onse osamala ntchitoyi uli mmanja mwawo.
Ntchito yomanga makiyosiki amadzi omwe ndi otetezeka a waterboard inayamba chaka chatha.