Anthu okhala m’mudzi mwa a Gulupu a Kaname mdera la Mfumu yayikulu Chilikumwendo m’boma la Dedza ati apindula ndi ntchito yolumikiza magetsi m’madera akumudzi ya Malawi Rural Electrification Programme (MAREP 9).
A Gulupu a Kaname ati anthu mderali, maka amayi, amayenda mtunda wautali kuti akapeze chigayo.
Iwo anaonjezera kuti kubwera kwa magetsi mdera lawo kwapereka mwayi kwa anthu okhala mderali kuti adzichita mabizinesi osiyanasiyana omwe akuti akuthandizira kutukula mabanja awo.

M’modzi mwa anthu ochita malonda ootchelera mderali, a Daiton Yeresoni, ati kubwera kwa magetsi mdera lawo kwawapindulira ponena kuti tsopano akukwanitsa kusamalira banja lawo kudzera bizinesiyi.
Ofalitsankhani mu unduna oona za mphamvu zamagetsi, a Austin Theu, wati boma lakwanitsa kulumikizitsa magetsi kwa mabanja oposa 200, m’sukulu komaso zipatala m’boma la Dedza kudzera mundondomeko yolumikizitsa magetsi ya MAREP 9.

A Theu ati mwa malo makumi awiri omwe akufuna kuwalumikizitsa ndi magetsi m’bomali, malo khumi ndi atatu awafikira kale ndi magetsiwa.
Iwo anaonjezera kuti boma, kudzera ku unduna wawo, lionetsetsa kuti madera onse m’dziko muno awalumikizitse ndi magetsi ndi cholinga chofuna kukwaniritsa masomphenya a dziko lino a Malawi 2063.
Padakali pano, anthu 25 pa 100 aliwonse ali ndi magetsi m’dziko muno ndipo boma likufuna kulumikizitsa magetsi kwa anthu 70 mwa 100 aliwonse pofika m’chaka cha 2030.