Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Local Local Music News Nkhani

Waluso asamatuwe ndi umphawi — Wendy

Mkulu wa Jacobs event, Wendy Harawa, wati chilichonse chili m’chimake pa chikonzero chofuna kubweretsa akatswiri akunja pankhani zamsangulutso kuti adzathandize aluso am’dziko muno za momwe angamachitire kuti adzitha kupindula ndi luso lawo.

Harawa wati ndizomvetsa chisoni kuti aluso ambiri m’dziko muno amakalamba asanadyelere luso lawo poti sadziwa njira zoti akhoza kutsatira kuti apambane ndi luso lawo.

Iye wati ichi ndichifukwa wakonza maphunzirowa.

Ena mwa akatswiri omwe adzakhale nawo ndi Mike Dada, yemwe ndi mtsogoleri wa Afrima Awards ndipo ndikadaulo wa zamalamulo, Ayo Animashaun yemwe ndi mkulu wa Headies Awards, smooth Promotions ndi Hip Tv Komanso Eric Belamy wa Live Nation: Paris, yemwe amathandizira kwambiri akatswiri akunja monga Beyonce, Jay Z, Drake akabwera ku Africa ndi enanso ambiri.

 

Related posts

Burning Spear abwera ku Malawi mu October Kudzaimba

Romeo Umali

MEC engages stakeholders on 2025 elections

Romeo Umali

NICE calls for mindset change in agriculture

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.