Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

USAID yatsanzika mwapamwamba ku Fisheries

Mawu oti pochoka pamsasa saipitsa ndi amene yagwira bungwe la USAID imene yapereka galimoto zitatu zandalama pafupifupi K380 million ndi katundu wina ku nthambi yoona za nsomba.

Galimotozi zimagwira ntchito mupulojekiti yazaka zisanu yobwezeretsa chilengedwe ndikuwonetsetsa kuti nsomba ya Chambo siikutha munyanja ya Malawi.

Malinga ndi a Daniel Jamu, mkulu wantchitoyi, galimotozi pamodzi ndi katundu wina zithandiza kupitsitsa patsogolo ntchito zanthambi ya Fisheries.

M’modzi mwa akuluakulu ku nthambi ya Fisheries, a Hastings Zidana, ayamikira USAID kudzera mu pulojekiti ya REFRESH kaamba kamphatsozi komanso ntchito yomwe agwira munyanja ya Malawi muzaka zisanuzi.

Kafukufuku waonetsa kuti Chambo chachuluka tsopano munyanja ya Malawi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Silver Strikers near unbeaten first round

MBC Online

‘Masewero ndi njira yofalitsa uthenga wa uchembere wabwino’

Simeon Boyce

MEC ikuunika zotsatira za chisankho

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.