Khonsolo ya mnzinda wa Blantyre yakhazikitsa ntchito yomanga zikwangwani zodziwitsa anthu kuti akulowa kapena kutuluka munzindawu.
Pokhazikitsa ntchitoyi kwa Kameza, mfumu ya mnzindawu, a Joseph Makwinja, anati kudziwa malile a mnzinda ndi kofunika kaamba kakuti adindo ndi anthu ena azidziwa kokapereka madandaulo koyenera.
Mu ntchitoyi, zikwangwani zisanu ndi chimodzi ndi zimene akuyembekezera kuzimanga m’mbali zonse za misewu ikuluikulu yolowa ndi kutuluka ku Blantyre monga ku Green Corner pamsewu opita m’boma la Chikwawa.
Ntchitoyi ndi ya ndalama zoposa K5 million ndipo ayigwira ndi thandizo lochokera ku kampani yopanga simenti ya Njereza.
Olemba: Naomi Kamuyango