Unduna wa za ulimi watulutsa mitengo yogulira mbewu chaka chino.
Malinga undunawu, chimanga chidzigulidwa pa mtengo osachepera K650, soya K800, thonje K900, nyemba zosasakanikirana K1200, nyemba zosakanikirana K900.
A Sam Kawale, omwe ndi nduna ya za ulimi, adalemba pa tsamba la m’chezo kuti mitengoyi ayikhazikitsa pambuyo pa zokambirana ndi mabungwe osiyanasiyana.
#MBCDigital
#Manthu