Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wapempha aMalawi kuti atengepo gawo pa ntchito yokonzanso chuma cha dziko lino mu njira zosiyanasiyana monga kulimbika pa ntchito za ulimi.
Dr Chakwera watinso anthu ochita malonda akuyenera akhale ndi mwayi ofanana potenga ngongole kuchokera ku bungwe la NEEF kuti ntchito zamtunduwu zipindulire anthu onse.
Mtsogoleri wa dziko linoyu wayankhula izi kwa anthu omwe anaima pa Katoto Roundabout ku Mzuzu.
Wolemba: Musase Cheyo