Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

Tiyeni tilimbikitse bata ndi mtendere — Chimwendo Banda

Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Richard Chimwendo Banda, wati bata ndi mtendere ndi zofunika kwambiri pamene dziko lino likukonzekera chisankho cha chaka cha mawa.

A Chimwendo Banda anena izi pa msonkhano umene iwo pamodzi ndi akuluakulu ena a chipanichi anachititsa pa sukulu ya Nasala kwa Malili m’boma la Lilongwe.

Iwo anati MCP imakhulupilira kuti mtendere ndi gwero la chitukuko cha dziko lili lonse, kotero n’kofunika anthu azikhala mwa mtendere komanso kulemekezana.

Pa nkhani ya chitukuko, a Chimwendo Banda anati mu kanthawi kochepa, boma la President Dr Lazarus Chakwera lagwira ntchito zosiyanasiyana za chitukuko kuphatikizapo kusintha mmene mzinda wa Lilongwe ukuonekera, ponena kuti tsopano uzioneka ndithu kuti ndi likulu la dziko lino, mwa ntchito zina zambiri.

Iwo analimbikitsanso anthu m’boma la Lilongwe kuti akalembetse m’kaundula wa chisankho kalembarayu akayambika Lachinayi sabata ino kuti akaponye ma voti ndi kusankha kuti chitukuko chipitilire.

 

Related posts

Malawi deserves easy access to financial investments — RBM

Romeo Umali

ISAMA hails MANEB for smooth PSLCE exams

Rabson Kondowe

‘Social Cash Transfer Programme will reach vulnerable people’

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.