Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Titangwanike pomanga dziko lino – Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wapempha  aMalawi kuti agwirizane ndi kuyenda limodzi ndi anthu omwe ali ndi chidwi chofuna kumanga dziko lino kuti chitukuko  chipite patsogolo.

Dr Chakwera anena izi pa bwalo la pasukulu ya pulaimale ya Hannock Msokera ku Kasungu pa mwambo wokondwelera kuti mpingo wa African Methodist Episcopal Church wakwanitsa zaka 100  ukugwira ntchito zake mdziko muno.

Mtsogoleri wa dziko linoyu wati  pali anthu ena omwe mmalo mothandiza kumanga dziko lino ndi kuona zabwino akupasula ndipo wapempha a Malawi kuti atangwanike pogwirizana ndi anthu  omwe  athandize kumanga dziko lino monga momwe a Hannock Msokera anachitira.

A Chakwera ati  dziko lino liri ndi vuto loiwala ndi kunyoza komwe tachokera  koma  watsindika kuti mpingowu ndi ofunika ndipo nkofunika kuwakumbukira  malemu a Hannock Msokera poti ati  ndi maziko a ufulu wa dziko lino  mu mbiri ya dziko lino.

Iwo ati mpingowu unathandiza Dr Hastings Kamuzu Banda kukapeza maphunziro a pamwamba Ku America zomwe ati zinabweretsa maziko a chitukuko cha chuma cha dziko lino komanso  maziko a ufulu omwe anthu akusangalala nawo mdziko muno.

Mmawu ake, mkulu wa mpingowu kuno ku Malawi, a Manuel Chamamba,  athokoza Dr Chakwera potsata m’mapazi a Dr  Banda, polemekeza mpingowu.  Iwo ayamikiranso mtsogoleri wa dziko lino pa ntchito za chitukuko monga zotukula migodi, ulimi ndi zokopa alendo zomwe akugwira komanso polimbana ndi mavuto omwe dziko lino likukumana nalo.

Mpingowu  anaukhazikitsa mdziko muno mchaka cha  1924 ndipo umathandizira boma m’magawo a zaumoyo komanso zamaphunziro.

Related posts

COURT ASKS ACB TO BE TRANSPARENT WITH EVIDENCE IN CHILIMA CORRUPTION CASE

MBC Online

MCP prioritises durable, quality projects – Gotani Hara

MBC Online

Tidziganizira momwe tingatukulire maanja athu — Kunkuyu

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.