Malawi Broadcasting Corporation
Development Local News Nkhani

Tisafalitse zopanda umboni

Nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati nkulakwira malamulo kumafalitsa nkhani zomwe zilibe umboni pankhani ya kusowa kwa ndege yomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima anakwera.

A Kunkuyu ati nthawi ino, ndi nthawi yoti tigwirane manja ndikupemphera ngati dziko kuti omwe akusaka ndege yi athe kubooleza.

Ndunayi yati bungwe la MACRA lalumikizana ndi mabungwe ena monga la ku Zambia komanso ku Angola kuti athandizire kupeza komwe ndege yi yagwera.

Iwo ati boma molumikizana ndi maiko ena achi ta chilichonse chothekera kusaka komwe ndege yi ili.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chikakula patuka, Ramadhan watumiza ‘leka’

Paul Mlowoka

Chenjerani namondwe akhoza kubuka panyanja yamchere

MBC Online

GOVERNMENT IMPRESSES EU

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.