Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

Timu ya Ekhaya ikusendera chifupi ndi ligi

Timu ya Ekhaya tsopano ili ndi mwayi waukulu olowa mu ligi yaikulu ya TNM kuchoka mu ligi ya mchigawo chakummwera pomwe tsopano ikungofuna ma poinsi awiri pamaseweronso awiri amene yatsalanawo.

Timuyi lero yagonjetsa timu ya Wanderers Reserve ndizigoli ziwiri kwa duu,  zimene zapangitsa kuti idzitsogola ndi ma poinsi asanu kutsatira kulepherana kwa matimu a Red Lions ndi Nyambadwe United pamasewero enanso omwe aseweredwa masana a lolemba.

Ekhaya ili ndi ma poinsi 28 pomwe Red Lions yomwe ndiyachiwiri ili ndi ma poinsi 23 ndipo onse atsala ndi masewero awiri kuti amalize ligi ya Thumbs Up.

Red Lions ikuyembekezeka kusewera ndi Ntaja United komanso Wanderers Reserve pamasewero ake omaliza pomwe Ekhaya yatsala ndi matimu a Nyambadwe United ndi Nyasa Big Bullets Reserve.

Ngati Ekhaya ingapambane masewero ake otsatira kapena kufananitsa mphamvu masewero onse awiri ndiye kuti ikhala akatswiri pomwe Red Lions ikuyenera kupambana masewero onse komanso kuti Ekhaya igonje masewero onse otsala kuti asilikali aku Zombawa abwererenso mu ligi ya TNM.

Related posts

MPs cheer as Chithyola announces CDF increment

Romeo Umali

Bullets gob-smacked as Wanderers book place in FDH final

Romeo Umali

CHAKWERA COMMITS $1M AT GLOBAL FUND’S 7TH REPLENISHMENT CONFERENCE

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.