Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Tidzagwira ntchito mwaukadaulo pa chisankho cha 2025, watero mkulu wa MBC

Mkulu wa bungwe lowulutsa mawu la Malawi Broadcasting Corporation (MBC), a George Kasakula, ati bungwe lawo lidzagwira ntchito mwaukadaulo ndi mopanda kukondera pa chisankho cha chaka cha mawa.

A Kasakula anena zimenezi ku Lilongwe pa zokambirana zokhudza ndondomeko zomwe bungwe la MBC lakonza zothandiza kuti lidzatumikire aMalawi popanda vuto.

Pa msonkhanowu pali alembi a zipani zosiyanasiyana monga MCP, DPP, UDF, Aford ndi zina zambiri komanso wapampando wa bungwe la atolankhani la Misa.

Related posts

Asanu agwidwa ataba zipangizo zomangira bwalo la timu ya Wanderers

Rabson Kondowe

Bande apempha mafumu atsogolere chitukuko

Blessings Kanache

Zipangizo za ulimi zifika msanga — Dr Chakwera

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.