Bungwe lolimbikitsa kuti amayi adzikhala m’maudindo akuluakulu la NGO Gender Cordination Network lati ladandaula kuti a Mary Navicha, omwe anali mtsogoleri wa aphungu a chipani cha DPP mnyumba ya malamulo sanawasankhe kukhala mtsogoleri otsutsa boma m’nyumbayi.
Wapampando wa bungweli, a Maggie Kathewera Banda, anena izi chipani cha DPP chitalengeza kuti chasankha a George Chaponda kukhala pa udindowu.
A Kathewera Banda ati iwo ndi anzawo akhala akuganiza kuti kaamba koti a Navicha akhala akugwirizira udindo otsogolera DPP mnyumba ya malamulo, komanso ngati njira yolimbikitsira amayi m’maudindo akuluakulu, amayenera kuwasankha kuti apitirize pa udindowu.
Akatswiri enanso a ndale monga a Chimwemwe Tsitsi komanso a Hawkins Munyenyembe, ati nawo amayembekezera kuti chipani cha DPP chisankha a Navicha chifukwa anaonetsa kale machawi popereka maganizo mosawopa ndi mosakondera pomwe amatsogolera aphungu a DPP mnyumba ya malamulo.
Olemba: Blessings Cheleuka


