Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

Kusayendetsa bwino chuma ku Netball kuopseza othandiza — NAM

Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa manja m’dziko muno la NAM lati kukanika kuyendetsa bwino chuma kumasewerowa kukuthamangitsa kampani zimene zili ndi kuthekera kokweza masewerowa.

Mlembi wa mkulu wa bungweli, a Yamikani Kauma, ndi amene ayankhula izi munzinda wa Lilongwe pa maphunziro a zachuma amene anakonza ndi a Old Mutual, omwe amathandiza masewerowa m’chigawo chapakati kudzera ku kampani yawo yotchedwa MPICO.

A Patricia Chatsika, m’modzi mwa akuluakulu a ku Old Mutual, anati cholinga cha maphunzirowa ndi kuthandiza osewera komanso oyendetsa masewerowa m’mene angagwiritsire ntchito ndalama.

Osewera ndi oyendetsa masewero a Netball okwana 100 m’chigawo chapakati ndi amene achita nawo maphunzirowa.

 

Related posts

Mphunzitsi amumanga pomuganizira kuti wagwilira ophunzira

Romeo Umali

6 FAMILY MEMBERS DIE IN ROAD ACCIDENT

MBC Online

Flames wapsa waku Guinea

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.