Achibale a malemu Dr Saulos Chilima apempha aMalawi kuti asiye kufalitsa nkhani zabodza zokhudza imfa ya m’bale wawo, zimene akuti ndi zowawawitsa mtima komanso zobweretsa mkwiyo pakati pawo.
Nsuweni wa Dr Chilima, a Joshua Valera, amayankhula izi pa Misa yapadera lero pa bwalo la Nsipe Catholic m’boma la Ntcheu ndipo anati ndi koyenera kulemekeza mzimu wa malemu Dr Chilima, amene anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, pokhala olimbika pa ntchito zotukula dziko lino.
M’mawu awo, Inkosi ya Makosi Gomani V, inati anthu m’dziko muno ayenera kukhala a chitsanzo chabwino m’magawo onse a moyo, monga momwe adaliri malemu Dr Chilima.
Pamwambo wa Misawu, akubanja la malemu Chilima apereka Mphatso ya mtanda ku Parish ya Nsipe, kumene Dr Chilima ankakonda kupemphera nthawi iliyonse imene amapezeka m’bomalo.