Anthu okhala mu nzinda wa Lilongwe omwe analembetsa mu ndondomeko ya Mtukula Pakhomo wam’mizinda akuyembekezeka kulandira ndalamazi lachinayi, zomwe ndi K150,000 aliyense.
Anthu 22 339 alandira mu gawo loyamba pamene gawo lachiwiri, anthu 16 329 ndiwo adzalandire ndipo gawo lachitatu adzalandira ndi anthu amene atatsale omwe salandira mmagawo awiri oyambilira.
Malinga ndi unduna wa zachuma ndi mapulani, ndalamazi cholinga chake ndikuthandizira anthu osowa amene akukumana ndi mavuto a zachuma.
Ku Zomba, Blantyre komanso Mzuzu, anthu analandira kale ndalamazi.