President wa dziko lino watsindika kufunika koti anthu m’dziko muno akhale ogwirizana komanso mwa bata ndi mtendere ndikuyika zonse mmanja mwa Chauta, pambuyo pa chiphyinjo chomwe chachitika m’dziko muno mwezi wathawu.
Dr Chakwera amalankhula ku Bingu International Convention Centre ku Lilongwe pa mapemphero apadera oyamika Chauta kuti dziko la Malawi lakwanitsa zaka 60 lili pa ufulu odzilamulira.
Iye anati akudziwa kuti anthu adakali mu ululu kaamba ka ngozi yomwe idachitika mwezi wathawu ndipo anapempha atsogoleri a mipingo kuti athandize kuthunzitsa aMalawi omwe mitima yawo ikadali yosweka.
Iye walangizanso apolisi kuti apitirize kugwira ntchito yawo mwaukadaulo kuti aliyense asamve kuphyinjika.
Dr Chakwera anati ali ndichikhulupiliro kuti lipoti lokhudza chomwe chidachititsa ngozi ya ndege likatuluka, lithandiza kutonthoza anthu.
Dr Chakwera anati tsopano pamene dziko la Malawi lakwanitsa zaka 60 lili la ufulu, anthu achilimike pa ntchito zosiyanasiyana zachitukuko komanso asamamvere anthu ena amene amangolimbikira ndale mmalo mwa chitukuko.
Iye anati kugwira ntchito za chitukuko, mmalo moganiza za ndale, ndikofunika kwambiri pokwaniritsa loto la Malemu Dr Saulos Chilima.
Pomaliza, iye anati adzipereka kutumikira aMalawi kuti dziko lino likwere.
Prezidenti Chakwera ndiye adalamula kuti pa mwambo wa chaka chino wa tsiku la ufulu odzilamulira, pachitike mapemphero okha basi, kuti anthu apemphelere Dr Chilima ndi ena asanu ndi atatu omwe adamwalira pa ngozi ya ndege mu nkhalango ya Chikangawa pa 10 mwezi wathawu.