Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, acheza ndi anthu m’madera angapo m’boma la Lilongwe, lero Lachitatu.
Dr Chakwera ayambira kucheza ndi anthu a kwa Chiuzira kenako kwa Pondamali, akachoka apo apita kwa Chiseka, kenako ku Mitundu, kwa Maluwa ndipo amaliza ndi kwa Kacheta.
Padakalipano, khwimbi la anthu lasonkhana kale pa Chiuzira kudikira kufika kwa President Chakwera.
Kudzera ku misonkhano imeneyi, mtsogoleri wa dziko linoyu afotokozera anthu ntchito za chitukuko zimene boma likugwira, komanso zimene likuchita powathandiza pa mavuto monga njala, komanso kumva mavuto ena amene anthu akukomana nawo.
Sabata zingapo zapitazi, Dr Chakwera anayendera anthu ku Nkhotakota, Dedza, Dowa, Mchinji ndi Kasungu.
Olemba: Isaac Jali