Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Pokhala pabwino ndipofunika msukulu’

Mmodzi kwa akuluakulu oona za maphunziro msukulu za m’madera akumidzi m’boma la Blantyre, a Alfred Mphandamkoko, wati malo ophunzira abwino komanso zipangizo zokwanira ndizofunika pokopa ana kuti adzipita ku sukulu komanso kuchita bwino pa maphunziro awo.

Mphandamkoko amayankhula pa sukulu yakatolika ya Mphati ku Machinjiri m’boma la Blantyre pomwe amalandira madesiki a ndalama zokwana K7 million kuchokera ku bungwe losungitsa ndi kubweleketsa ndalama la Polymed Sacco Limited.

Iwo anati pakadali pano boma lili mkati moonjezera midadada yamakalasi msukulu ndipo Mphati ndi imodzi mwa sukulu zimene zipindule ndi ntchitoyi.

Pamenepa iwo apempha mabungwe enanso akufuna kwabwino kuti athandizenso sukuluyo ndi mipando ina pomwe zipinda zophunzilira zikuchuluka.

Polymed Sacco yapereka madesiki  akuluakulu okwana makumi asanu.

 

Olemba: Naomi Kamuyango

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHAKWERA TO MEET FORMER HEADS OF STATE OVER CYCLONE FREDDY

McDonald Chiwayula

British Govt reaffirms support for meteorological services

Charles Pensulo

KUHes, CARTA to address postgraduate study challenges

Lonjezo Msodoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.