Nduna ya za madzi ndi ukhondo yomwenso ndi phungu oimira dera la Chikwawa Mkombezi, Abida Mia, lero anayendera zitukuko zomwe akhazikitsa posachedwapa kuphatikizapo mijigo yokwana isanu ndi iwiri yomwe yakumbidwa mderali.
Poyankhula pa bwalo la Mfumu Mpoza pomwe ndi amodzi mwa malo omwe akumba Mjigo watsopano, a Mia ati ndicholinga cha mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti paliponse pakhale chitukuko.
Ndipo polankhulapo mfumu yaing’ono Tsalabeni yati zitukuko zomwe akhazikitsa mderali kuphatilizapo sukulu, komanso chipatala zithandiza kuchepetsa mavuto osiyànasiyana omwe derali limakomana nalo.
Iwo apempha anthu mderali kuti ayende limodzi ndi phungiyi kuti chitukuko chipitilire mderali.
Ayisha Misi yemwe ndi mkulu oimira Malawi Relief Fund, bungwe lomwe likuthandiza zitukuko mderali ati ndiwokodwa kuona kuti nasomphenya a Mia otukula derali akukwanilitsidwa.
Olemba: Telson Magombo