Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Oyendetsa galimoto wadzipereka atapha anyamata atatu

Anthu atatu afa ndipo m’modzi akulandira thandizo la ku chipatala galimoto la mtundu wa Mazda Axela Hatchback litawagunda Lolemba m’mawa m’boma la Mangochi.

Ofalitsankhani wa polisi ya m’chigawo cha ku m’mawa, a Patrick Mussa, ati anthuwa anali pa mwambo wa chinamwali pa mudzi wa a Ndege pafupi ndi sitolo za pa Mpale kwa mfumu yayikulu Chimwala m’bomalo.

Atatuwa anavulala kwambiri m’mutu ndipo amwalira akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Ukalanga. Winayo wavulala kwambiri miyendo ndipo akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha chikulu cha Mangochi.

A Mussa ati amene amayendetsa galimotoyo, a Frank Nguni, 29, anathawa ndi kusiya galimoto lawo pamalo angoziyo koma kenaka anakadzipereka yekha ku polisi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Osagwiritsa ntchito imfa ya malemu Dr Chilima pa zifukwa za ndale’

Paul Mlowoka

‘Government is trying to restore, protect natural resources’

MBC Online

Tobacco earnings hit month-long import cover

Justin Mkweu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.