Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

‘Pewani m’chitidwe ogwiritsa ntchito ana’

Apolisi ku Chileka mu mzinda wa Blantyre amanga anthu anayi powaganizira kuti amatuma ana kuti adziwagulitsira malonda nthawi ya sukulu.

Ofalitsa nkhani ku Polisi ya Chileka, a Phillipo Jonathan, anati kutero ndi kuphwanya ufulu wa ana.

A Phillipo anaonjezeranso kuti amanga anthuwo potsatira kuchuluka kwa ana amene amapezeka akugulitsa malonda pa sitolo za ku Lunzu nthawi imene ndi ya sukulu.

Kutsatira izi, apolisi apulumutsa ana 42 ku m’chitidwe umenewu ndipo ena awatumiza kwa makolo awo.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mudzi wa aChewa autsekulira ku Lilongwe

MBC Online

UNDP offers advice to foster SME growth in Malawi

Salomy Kandidziwa

Chikondwelero chasefukira kwa anthu aku Mapuyu South pakukhazikitsidwa kwa ntchito ya msewu

Eunice Ndhlovu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.