Boma la Neno likuchita bwino pa ntchito yolimbana ndi kachirombo koyambitsa matenda a edzi, kudzera mu ndondomeko yotchedwa HIV/AIDS Intergrated Initiative, bungwe la National Aids Commission (NAC) ndi mabungwe ena atsimikiza.
Akuluakulu a NAC pamodzi ndi mabungwe ena anayendera chipatala cha bomali pofuna kuona momwe ndondomeko yatsopanoyi ikugwilira ntchito.
Padakali pano, boma la Neno latsitsa chiwerengero cha ana amakanda omwe amatenga kachiromboka kuchokera kwa mayi awo ndi 98%.
Mkulu owona za umoyo m’boma la Neno, a Dr. Albert Chafunya, ati chipatalacho chikukwanitsa kufikira anthu ochuluka ndi thandizo la chipatala m’bomali kaamba kakuti limachilimika komanso kuika chidwi pa nkhani yodziwitsa anthu powafikira m’madera mwawo.
Wapampando wa Board ya NAC, a Chipo Kanje, anati n’zokondweretsa kuona kuti ndondomeko zomwe Chipatala Cha boma la Neno chikutsata zikubereka zipatso zabwino.