Bwalo la Magistrate mumzinda wa Lilongwe lagamula kuti nzika zitatu zadziko la China zikakhale mndende kwa zaka zisanu ndi chimodzi atazipeza olakwa pa mlandu ozembetsa anthu.
Awiri mwa anthuwa, amene ndi abambo, Zhang Yan Qing ndi Zhou Yan Hu, awapeza kuti sadatsate ndondomeko zoyenera pamene amafuna kutenga ngati banja amayi awiri akuno ku Malawi kudzera ku ofesi ya bwanamkubwa.
Nzika inanso yaku China, mayi Mian Mian Chen, akuti ndiyo idawasunga anthu anayiwa pakhomo pake kwa sabata ziwiri pamene amayembekeza kunyamuka m’dziko muno ulendo waku China.
Anthuwa anagwidwa pabwalo la ndege la Kamuzu International ndi apolisi.
Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ku Central West Region, a Foster Benjamin, atatuwa agwira ukayidi m’dziko mom’muno.
#MBCOnlineServices
#inspiringthenation