Nzika ya ku Niger, a Osman Muhammad, akuyisunga ku ndende ya Maula khoti litakana pempho lake la belo.
Lachitatu masana, Muhammad anakaonekera kubwalo la Magistrate la Mkukula ku Lumbadzi pa mlandu opezeka ndi mankhwala oopsya amene ali ozunguza ubongo komanso ofuna kuzembetsa mankhwalawa kudzera m’dziko muno.
Malinga ndi ofalitsankhani wa Polisi ya KIA, a Sapulain Chitonde Lee, mlanduwu ukhala ukupitilira Lachisanu pa 10 May pa bwalo lomweli.
A Muhammad adawapeza ndi mankhwala oopsya komanso ozunguza bongo pa bwalo la ndege la KIA pamene amafuna kuti pite m’dziko la Germany.
Iwo adawapeza ndi mankhwala otchedwa Diamorphine okwana 51 omwe adawabisa mu zikwama zawo ndi ena okwana 13 amene anali kumalo okhalira.
#MBCDigital
#Manthu