Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Sports Sports

Takonzeka kuthetsa mbiri ya Bullets — Chimimba

Mkulu wa timu ya Silver Strikers, Patrick Chimimba, wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets isawayang’anire pansi potengera mbili yoti chaka chatha yatenga zikho zonse poti tsopano iwo akonzeka mokwana.

A Chimimba anena izi pamwambo omwe kampani ya NBS Bank imapereka ma yunifolomu amene matimuwa adzavale pamasewero awo loweruka pa Bingu National Stadium mu mpikisano wa Charity Shield.

“Iyi ndi season ina ndipo ife takonzeka kulemba mbiri yatsopano,” watero Chimimba.

Mlembi wamkulu wa masapota a timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Alchibald Kasakula, wati Silver ikuyenera kudziwa kuti bullets yapambana kale masewero omwe akhaleko lowerukawa ndipo chomwe chatsala ndikulandira mphoto yawo.

Mwambo opereka ma yunifolomu ku matimuwa unachitikira ku Bingu National Stadium ndipo akulu akulu a ku NBS Bank komanso Football Association of Malawi ndiomwe anatsogolera zonse.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Alimbikitsa anthu kupha makwacha kuchokera ku zinyalala

Aisha Amidu

Habitual thief sentenced to eight years in jail

Romeo Umali

TIME TO SPEAK TRUTHFULLY WITH EACH OTHER – CHAKWERA

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.