Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Local Nkhani

Mwambo wa Sand Music siukhalapo chaka chino

Mwambo wa Sand Music Festival wa chaka chino siukhalapo chifukwa cha imfa ya ‘Soldier’ Lucius Banda, amene anali mkulu wa kampani imene imakonza mwambowu ya Impakt Events.

Mwambowu umayenera kuchitika kuyambira pa 27 mpakana pa 29 September chaka chino m’boma la Mangcohi.

Mu kalata, yomwe MBC Digital yapeza, Impakt Events yati ikulirabe imfa ya Lucius Banda ndipo mwambowu ubweleranso chaka cha mawa kuyambira pa September 26 mpaka 28.

Banda pamodzi ndi gulu loyimba la The Black Missionaries ndi amene anayambitsa mwambo wa Sand Music Festival pofuna kuoonetsetsa kuti oyimba achiMalawi akukhala ndi mwayi owonetsa luso lawo komanso kupeza phindu pa luso lawo.

Lucius Banda adamwalira pa 30 June chaka chino m’dziko la South Africa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Kabaza operators welfare key in supporting their marriages

Sothini Ndazi

“Osanyoza anthu achikulire” — Chakwera

Romeo Umali

Late header sinks Wanderers

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.