Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Mwambo wa Kulamba ulipo chaka chino

Bungwe la Chewa Heritage Foundation (CHEFO) lati chaka chino mwambo wa Kulamba ukhalapo ku Mkaika m’boma la Katete mdziko la Zambia.

Yemwe akulumikizitsa mafumu pankhani za Kulamba mmaiko a Malawi, Zambia komanso Mozambique, a Senior Chief Lukwa alengeza izi m’boma la Lilongwe pamnsonkhano wa atolankhani.

A Senior Chief Lukwa ati pokonzekera mwambo waukulu wa kulamba wa chaka chino pakhala zochitikachitika zikuluzikulu ziwiri. Iwo ati pa 26 July 2024 akonza  mwambo omwe anthu akufuna kwabwino akuyenera kudzathandiza bungweli ndi ndalama pokonzekera mwambo wa Kulamba.

Iwo atinso bungwe la CHEFO lagula malo okwana maekala khumi omwe ali mmudzi wa msampha kwa mfumu yaikulu Chadza m’boma la Lilongwe. Pa malowa ati akufuna pakhale wailesi youlutsa mawu, malo ochitira magule osiyanasiyana komanso misonkhano.

A Senior Chief Lukwa ati sadzasekerera aliyense yemwe adzapezeke  akuchita zaukamberembere posonkhetsa ndalama m’dzina la bungweli. Iwo ati pali dongosolo lomwe akonza losonkhetsera ndalamazi ndipo omwe adzagwire ntchitoyi adzakhala ndi ziphaso zochokera ku bungweli.

Mwambo wa Kulamba udzachitika  pa 31 August 2024 ndipo bungweli likuitanira anthu a mitundu yonse ku mwambowu.

Pamsonkhawu panali mafumu a ndodo monga Senior Chief Khongoni, Senior Chief Mbwatalika, Senior Chief Chadza  a m’boma la Lilongwe, Senior Chief Nthondo a m’boma la Ntchisi ndi a Senior Chief Dambe a m’boma la Mchinji.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Aphungu otsutsa akukana kukambirana za lamulo losintha kagulidwe ka mafuta agalimoto m’dziko muno

MBC Online

FAO pushes for digital tools in farming field

Yamikani Simutowe

KAWINGA FC CLINCH CHIPIKU LEAGUE TITLE, EARN SUPER LEAGUE PROMOTION 

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.