Bungwe la Malawi Gaming and Lotteries Authority ( MAGLA), lachenjeza kuti lamulo ligwira ntchito kwa makolo omwe amalimbikitsa ana awo kuchita juga.
Mkulu wa bungwe la MAGLA a Rachel Mijiga ati ndi kuphwanya malamulo kulola mwana ochepera zakha 18 kuchita nawo masewero-wa.
A Mijiga amafotokoza izi lachisanu, pa mwambo obzyala mitengo mu mzinda wa Lilongwe.
Bungwe la MAGLA ndi bungwe lomwe limaonetsetsa kuti anthu komanso makampane azitsatira malamulo a juga.
Olemba: Tasungana Kazembe.