Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Mneneri ali mchitokosi

Apolisi m’boma la Chiradzulu atsekera mneneri wa chizimai Jessie Windo wa zaka 74 pomuganizira kuti wavulaza pothyola miyendo ya bambo wina yemwe anapita kuti akamuchiritse pomupempherera.

Wofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chakumpoto chakuvuma, a Edward Kabango, atsimikiza za nkhaniyi.

A Kabango ati a Windo anapalamula mlanduwu pa 16 mwezi uno m’mudzi wa Mangira m’boma la Chiradzulu komwe mneneriyu anathyola miyendo ya bambo wina wodwala pomwe amaiongola atamaliza mapemphero kuti achire.

Apolisi ati a Windo akaonekera ku bwalo la milandu posachedwa. Mneneriyu amachokera m’mudzi wa Nyandero, mdera la mfumu yaikulu Malemia m’boma la Nsanje.

Olemba: Alufeyo Liyaya.
#MBCDigital
#Manthu

Related posts

FMB Capital Holdings yapanga phindu lokwana K137.8 billion

Rabson Kondowe

Police calls for support against mob justice

Romeo Umali

BOMA LAPEZA MISIKA YAMBIRI YAMBEWU ZA ALIMI

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.