Bungwe loona za chisankho mdziko muno la MEC lati kalembera wa chisankho cha makhansala chomwe chichitike pa 23 June 2024 ku ma ward a Mwasa m’boma la Mangochi ndi Chilaweni m’boma la Blantyre iyamba lolemba 10 June mpaka Lamulungu pa 16 June 2024.
Ofalitsa nkhani za Bungwe la MEC, a Sangwani Mwafulirwa, ati malo ochitira kalemberawo adzitsegulidwa 8 koloko mmawa ndi kuwatseka 4 koloko madzulo.
Iwo ati anthu omwe analembetsa maina awo mu kaundula oponya voti akuyenera kukatsimikiza ngati main awo alimo mu kaundulayo ndipo ena amene anataya ziphaso zoponyera voti akuyenera kupita ku malo olembetserawo kuti akawapatse ziphaso zina zoponyera voti.
A Mwafulirwa ati amene analembetsa mu kaundula wa chisankho chomwe chimayenera kuchitika ku Mwasa Ward chaka chatha chomwe chinalephereka akuyenera kukalembetsanso chifukwa maina awo sanalowe mukaundula wa anthu oyenera kuponya voti.