Apolisi ku Mulanje amanga m’busa wina, Steven Zambia, wazaka 38, pomuganizira kuti wakhala akugwililira mtsikana wazaka 15 kuchokera mwezi wa February mpaka June chaka chino pomunamiza kuti amuchiritsa matenda a khunyu omwe akudwala.
Mneneri wa apolisi ku Mulanje a Innocent Moses ati makolo a mtsikanayo akhala akuyitana anthu opemphera kuti adzamupemphelere mwana wawoyo. Koma M’busa Zambia anauza makolo a mtsikanayo kuti amutenga azikamupemphelera kunyumba kwake. Koma atapita kunyumbako, m’busayo amagona naye mpaka kumupatsa mimba.
Atawona kuti mtsikanayo ndi woyembekezera, m’busayo ananyengelera makolo ake kuti angomukwatira mwana wawoyo, zomwe sizinasangalatse makolowo ndipo anakanena ku polisi.
M’busa Zambia ndi wa m’mudzi wa Makaula mfumu yaikulu Mabuka m’boma lomwelo la Mulanje.