Bungwe la Spinal Injuries Association of Malawi (SIAM) lapempha adindo a ntchito za boma kuti adzimanga ofesi zimene zikhoza kulola anthu awulumali ovutika ndi kuyenda kuti adzitha kupitako ndi kupeza thandizo mosavuta.
Bungweli ndi la anthu amene ali ndi ulumali wa msana umene unadza kaamba kovulala.
Wapampando wa SIAM, a Byton Kondowe, ndi amene anapereka pempholi lero masanawa mu mzinda wa Lilongwe, pamene bungweli limachititsa maphunziro a lamulo lomwe limatchedwa kuti Access to Information (ATI) m’chingerezi.
Lamuloli limakakamiza nthambi, maunduna, mabungwe a boma ndi amene siaboma kuti azipereka uthenga kwa anthu omwe afuna kudziwa zinthu.
M’modzi mwa adindo ku bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC), a Chance Kalolokesya, amene amadzwitsa za ATI, anayamikira bungwe la SIAM poonetsa chidwi pofuna kuphunzila lamuloli.
A Kalolokesya anapempha bungweli kuti likhale patsogolo popereka uthenga okhudza ntchito zawo kwa anthu m’dziko muno poti aliyense ali ndi ufulu oti adzitha kupeza uthenga mosavuta, malinga ndi malamulo a dziko lino pa gawo 37.
Mubajeti ya chaka chino, MHRC inapatsidwa ndalama zoposa K100 million zogwilitsira ntchito yodziwitsa anthu lamulo la ATI.
Koma a Kalolokesya ati ndalama zimene angafune pachaka zimayandikira K1 billion ndipo iwo akuvutika magwiridwe awo a ntchito chifukwa thandizo la ndalama likuchepa.
Lamulo la ATI analivomereza m’chaka cha 2017 ndipo linayamba kugwira ntchito m’chaka cha 2020.