Majaji m’dziko muno ati ali ndi chisoni kaamba ka imfa ya a Raphael Kasambara omwe anali katswiri wa za malamulo komanso yemwe anathandiza kwambiri polimbikitsa ntchito zamalamulo m’dziko muno.
Justice Zione Ntaba, anena izi pamwambo otsanzikana ndi a Kasambara omwe ukuchitikira kunyumba kwa malemuwa ku Nyambadwe mu mzinda wa Blantyre.
Posachedwapa, maliro apita nawo ku CI komwe kukachitikire mapemphero asananyamule thupi la Malemuwa pa ndege kupita kumudzi kwawo m’boma la Nkhata Bay komwe akaliyike m’manda lolemba.
A Michael Usi, nduna yazosamalira chilengedwe, ndiwo akuimira boma pa mwambowu.