Mphunzitsi watimu yadziko lino yamasewero ampira wamiyendo ya Flames, Patrick Mabedi, wati gulu lomwe timuyi yapezekamo pofuna kudzigulira malo kumpikisano wa Africa Cup of Nations ndilovuta.
Malawi ili mu gulu L limodzi ndi matimu a Senegal,Burkina Faso komanso Burundi.
Mabedi wati timuyi ikuyenera kukonzekera mokwanira kuti idzachite bwino m’masewero amene aseweredwe miyezi ya September, October ndi November chaka chino.
Senegal ndiwo anali akatswiri a AFCON 2021 pomwe Burkina Faso yapezekamo kumpikisanowu kokwana ka 13.
Olemba: Praise Majawa