Apolisi anjata a Stanley Chirwa, amene ndi oyimira anthu pamilandu (lawyer), powaganizira kuti ali ndi galimoto la mtundu wa Ford Ranger limene lidabedwa ndi zigawenga za mfuti m’dziko la South Africa, m’chaka cha 2018.
Mneneri wa apolisi m’dziko muno, a Peter Kalaya, ati galimotoyi a Chirwa anapita nayo kokayilembetsa pa 8 April 2024, koma iwo anapeza kuti galimotoyi ikufanana ndi yomwe idabedwa ndi mbala zaku South Africa, malinga ndi zopeza za apolisi a m’dzikolo.
A Kalaya ati bambowa akukanika kufotokoza komwe iwo adagula galimotoyi koma ati apolisi afufuza kuti apeze choonadi.
A Chirwa akuyembekezeka kuwatsekulira milandu ingapo, kuphatikizapo kulandira kapena kubweretsa katundu wakunja popanda chilungamo, komanso kupezeka ndi katundu amene akumuganizira kuti ndi obedwa.