Ligi ya masewero a Volleyball ya achisodzera ati ipitilira mwezi ukaoneka pa 11 April, pofuna kuti masewerowa adziyendera limodzi ndi chikhalidwe komanso zikhulupiliro.
Lachitatu, bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM) linati mwezi otsiriza kusala kudya wa Ramadan sunaoneke, choncho Eid idzakhalapo lachinayi.
A Frank Makowa, Mlembi wa ligiyi, yomwe dzina lake ndi Classic Under 20, ati mpikisanowu ukuyenera kutha malinga ndi m’mene mwezi uonekere.
#MBCDigital
#Manthu