Dziko la Malawi, pamodzi ndi maiko ena onse padziko lapansi, lero akukumbukira tsiku la matenda a kadzamkodzo, amene pachingelezi amatchedwa kuti Fistula.
Tsikuli layamba ndi ulendo wa ndawala ozungulira chipatala cha Bwaila mu mzinda wa Lilongwe pamene anamwino, odwala matendawa komanso adindo ena akuyimba nyimbo komanso kuvina.
Tsikuli amalikumbukira pa 23 May chaka chili chonse pofuna kuwunikira ntchito yolimbana ndi matendawa.