Nthambi ya bungwe la Southern African Alcohol Policy Alliance (SAAPA) yomwe ili m’dziko muno yati pakufunika malamulo okhwima kuti mchitidwe okumwa ndi kufulula mowa mwa chisawawa pakati pa achinyamata uthe.
A Jefferson Milanzi, omwe ndi wapampando wa SAAPA, ndiwo ayankhula izi pamsonkhano osankha komiti ya bungweli.
“Malawi 2063 ili m’manja mwa achinyamata omwe akupopa bibida mopyola muyeso! Ndipovuta kuti ugwire ntchito zachitukuko, nanga 5 koloko m’mawa munthu waledzera kale?” atero a Milanzi.
A Munila Bakali, omwe awasankha ngati wachiwiri kwa mkulu wa komitiyi, anati mabanja ambiri m’dziko muno akusokonekera kaamba ka mchitidwewu, zomwenso zimasokoneza maganizo angwiro.
Posachedwapa, anthu oposa asanu anamwalira kwa Manase munzinda wa Blantyre atapapira mowa oopsa otchedwa ‘Ambuye tengeni’.