Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Kulowetsa galimoto mozemba ndi mlandu

Bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority MRA lati likukumana ndi mavuto pa ntchito yotolera misonkho, maka pa galimoto zimene zimalowa m’dziko muno mozemba.

Mkulu wazamalonda ku bungweli, a Wilma Chalulu, wati anthu ena samafuna kuti galimoto zawo azifufuze ngati analipira msonkho kapena ayi polowa m’dziko muno.

A Chalulu apempha olembankhani kuti athandize kudziwitsa anthu zakufunika kopereka msonkho pa galimoto polowa mdziko muno komanso kupereka mpata ku bungweli kugwira ntchito mosavuta yofufuza galimoto zamtunduwu.

Boma limagwiritsa misonkho munjira zosiyanasiyana monga kumanga misewu, sukulu, zipatala, nyumba za ogwira ntchito m’boma komanso kupereka malipiro awo.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Osagwiritsa ntchito imfa ya Chilima pa ndale

MBC Online

Baba Malondera lauds Chakwera’s administration

MBC Online

BWALO LA MILANDU LABWEZA GALIMOTO YA UMBONI WABOMA

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.