Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Kulimbikitsa ngodya zisanu zamaphunziro

Unduna wamaphunziro wati ukuika chidwi kwambiri pa ngodya zake zisanu zokweza maphunziro kuti maphunziro akhale opindulira ophunzira.

Mlembi wankulu mu Unduna wazamaphunziro a Mangani Katundu wauza MBC kuti mwazina, ngodya zisanuzi zikulunjika pa nkhani yowonetsetsa kuti aphunzitsi akupeza zosowa zawo komanso akuchita maphunziro oyenera asanawalembe ntchito, Kusinthanso ndondomeko ya maphunziro kapena kuti curriculum, kuonesetsa kuti ntchito yogawa phala ifikile sukulu zonse mdzikomuno komanso kulimbikitsa luso lamakono pakati pa ophunzira.

Powonjezera apa, a Katundu ati Unduna wazamaphunziro ukuyesetsanso kuti ophunzira 700,000 omwe analibe mwai ophunzira mzipinda zolongosoka akhale ndi mwayi umenewo kudzera ku ndondomeko Malawi Education Reform Programme (MERP) yomwe yaika padera ndalama zokwana K150 billion zomangira zipinda zamakono zophunziliramo.

 

By Tasungana Kazembe

Related posts

‘LET’S PRESERVE HERITAGE SITES’: A CALL FOR COLLABORATION

MBC Online

GOVT PLEDGES TO SUPPORT CREATIVE INDUSTRY

MBC Online

CDF can transform rural areas-Mwalwanda

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.