Akuluakulu a khonsolo ya m’boma la Nkhotakota ati kulandira kwa ndalama zachitukuko mopelewera komanso mopanda ndondomeko kukusokoneza magawo ambiri akagwiridwe kawo kantchito m’bomali.
DC wa bomali, a Ben Matengeni Tonho, wanena izi Ku nyumba ya malamulo pomwe komiti yoona za maboma aang’ono komanso chitukuko cha mmidzi inawayitsanitsa kuti akamve mavuto omwe akukumana nawo.
Iwo ati akhala akukumana ndi mavutowa kuyambira m’chaka cha chuma cha 2023 mpaka 2024 ndipo ati akhala akuvutika kugula zinthu zofunika pa khonsolo, kulipira ma khansala komanso kulipira ma bilu, mwa zina.
Wapampando wa komitiyi, a Horace Chipuwa, yemwenso ndi phungu wa Lilongwe Mapuyu, watsimikizira khonsoloyi kuti apititsa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo.