Oyimba nyimbo zauzimu amene akonza mwambo wamaimbidwe ndi cholinga chothandiza nzawo Peter Uyu Mlangeni, yemwe adavulala pangozi yagalimoto, ati pakufunika K15 Million kuti Mlangeni alandire thandizo lachipatala loyenera.
Polankhula kwa atolankhani ku Lilongwe, m’modzi mwa oyimba amene akutsogolera chikonzerochi, a Norman Phiri, ati Mlangeni anavulala fupa la pamsana, limene pachingerezi limatchedwa spinal cord.
Oyimbawa ati akhala akuyesetsa kuthandizana ndi Mlangeni koma pano achiona chanzeru kuti achipereke kwa a Malawi kuti nawonso awonetse chikondi chawo pobwera ku phwandoli pamtengo osachepera K3000.
Mneneri wa gulu la oyimbawa, Precious Chikatiko, wati pakadali pano atolerako ndalama zoposa K800,000 ndipo apempha akufuna kwabwino kuti athandizepo.
Ena mwa amene adzayimbe nawo pamwambowu ndi Skeffa Chimoto, Great angels choir, Lulu, Shammah vocals, Kondwani Chirwa komanso King James Phiri.