Anthu omwe amasungitsa ndalama zawo mu banki zosiyasiyana m’dziko muno akhala ndi chitsimikizo chochuluka cha chitetezo pa nthawi yomwe bank zingalephere kupitiriza ntchito.
Izi zili chomwecho chifukwa boma lidakhazikitsa nthambi yotchedwa Deposit Insurance Corporation (DIC) imene aitsekulire sabata lamawa.
Nthambiyi anayikhazikitsa kudzera mu lamulo kuti idzipereka insurance kwa kampani zosunga ndalama, ndicholinga choteteza anthu osungitsa ndalamazo.
Poyankhula pa maphunziro a olembankhani zamalonda ndi chuma, mkulu wa nthambi ya DIC, a Chitani Chigumula, ati malinga ndi lamulo la DIA, banki zonse zomwe zili ndi chiphaso zikuyenera kukhala pa sikimu yomwe zidzidulidwa ndalama yolingana ndi kukula kwa chiwerengero cha ndalama zomwe akusunga.