Bwalo lamilandu ku Zomba lalamula mwamuna wazaka 55, Bamus Wilesi, kukakhala kundende zaka 16 atapezeka wolakwa pamlandu ogwililira mtsikana wazaka 14 yemwe anamupatsa K2,000 kuti asawulure.
Ofalitsankhani wapolisi ku Zomba, Patricia Sipiliano, wati mtsikanayo amakonda kudutsa pakhomo pa Wilesi, yemwenso ndi sing’anga, popita kukatunga madzi komanso ku chigayo.
Tsiku lina, sing’angayo ananyengelera mwanayo ndikugona naye kenako anamupatsa ndalamayo ngati chitseka pakamwa.
Koma atafika kunyumba kwawo, mtsikanayo anatulutsa ndalamayo kunyaditsa amzake makolo ake akuwona.
Atamufunsa, iye anaulura za nkhaniyo.