Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Sports Sports

Chipala, Kamwendo awonetse ukadaulo wawo — Chemis

Otsatira masewero a mpira wa miyendo, Dan Chemis, akukhulupilira kuti osewera wa Silver Strikers, Charles Chipala, komanso wa Premier Bet Dedza Dynamos, Promise Kamwendo, akhala akufuna kuti awonetse ukadaulo wawo matimu awiriwa akakumana mu mpikisano wa Airtel Top 8 Lachitatu masana ku Lilongwe.

Pa 14 February chaka chino, Chipala adasayinira mgwirizano wazaka zitatu ndi timu ya Silver Strikers kuchokera ku Dedza Dynamos ndipo wakwanitsa kumwetsa zigoli zokwana zisanu m’mipikisano yonse.

Koma a Chemis anati Promise Kamwendo, osewera wa Dedza, nayenso akhala akufuna kuti asewere bwino kuti asangalatse amene angafune ntchito yake mtsogolomu, popeza mgwirizano wake ndi timuyi ukhala ukutha posachedwa.

Mphunzitsi wa Silver Strikers, a Peter Mponda, anati masewero amene akudzawa akhala ovuta zedi chifukwa masewero adzikho zapambali pa ligi yayikulu china chilichonse chikhoza kuchitika.

A Mponda anapereka chitsanzo m’mene iwo adagonjera ndi timu ya Blue Eagles mu chikho china, koma anatibe ayesetsa kuti agwiritsire ntchito bwalo lawo la Silver ku Area 47 mu mzinda wa Lilongwe ndi cholinga chakuti ntchito ichepe.

Mbali inayi, mphunzitsi wa Dedza Dynamos, a Andrew Bunya, ananenetsa kuti iwo achita zothekera kuti akagonjetse Ma Banker pa bwalo lawo lomwero ngakhale akudziwa kuti sakakhala masewero ophweka.

A Bunya anati sakufuna kuti m’masewero a chibwereza adzakhale ndi phuma.

Silver Strikers ndi Dedza Dynamos akachotsana chimbenene Lachitatu, adzakumamananso pa 20 October pa bwalo la Dedza m’masewero achibwereza pofuna kupeza katswiri amene adzapite mu ndime ina ya mpikisanowu.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Wanderers yavomereza Mwase

MBC Online

Govt assures Malawians of improved livelihoods

MBC Online

God’s Grace Academy celebrates Africa Day

Chisomo Break
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.