Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Bangwe yapha Bullets

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yagonja ndi timu ya Bangwe All Stars 1-0 pa bwalo la masewero la Kamuzu kudzera mu chigoli cha James Msowoya.

Aka ndi kugonja kachitatu kwa Bullets mu 2024 TNM Super League imene ili pa nambala khumi pa mdandanda wa matimu amu ligiyi.

Kupambanaku, zikutanthauza kuti Bangwe tsopano ili ma nambala 15 pa mdandanda wa matimuwa ndi ma point okwananso 15.

Awatu ndi masewero oyamba kuti timuyi igonjetse amene akusungira chikhochi komanso koyamba kuti achinye pagolo pawo pamasewero asanu amene asewera limodzi.

Komanso, awa anali masewero achiwiri a Trevor Kajawa chilhalireni ngati mphunzitsi wa tsopano wa Bangwe.

 

Olemba: Praise Majawa

Related posts

MP urges churches to combat rising suicide cases

Rabson Kondowe

Vendors snub SULOM on beverages

Romeo Umali

Man jailed on suspicion of murdering wife

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.