Apolisi m’boma la Mchinji ati bambo Frank Phiri azaka 46 amwalira pangozi yamoto m’boma la Mchinji zigubu zamafuta agalimoto zimene amasunga m’nyumba yawo zitakolera moto.
Ofalitsankhani za polisi ya m’bomali, a Limbani Mpinganjira, ati malemuwa akhala akuchita malonda amafuta agalimoto amene amawasunga mukantini imene inalumikizana ndi nyumba imene amagona.
A Mpinganjira anati motowu udayamba pa tsiku limene bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) linali pakalikiliki kutseka malo omwetsera mafuta agalimoto kaamba kogulitsa mafuta m’zigubu.
A Phiri anavulala kwambiri komanso katundu wawo yense adatha psiti ndipo anthu akufuna kwabwino anathamangira nawo ku chipatala chachikulu cha Mchinji ndipo anawasamutsira ku chipatala cha Kamuzu Central munzinda wa Lilongwe kumene amwalira akulandira thandizo.
Chifukwa cha ichi, apolisi alangiza anthu kuti apewe kuchita malonda ogulitsa mafuta agalimoto m’zigubu, amenenso ndi oletsedwa ndipo atsatire malamulo a MERA.
Malemuwa anali a m’mudzi mwa Sawala kwa mfumu yayikulu Mkanda m’boma la Mchinji.