Achinyamata awalangiza kuti asaononge tsogolo lawo polola kuti andale adziwagwiritsa ntchito yoyambitsa ziwawa pamene dziko lino likukonzekera chisankho m’mwezi wa September chaka chino.
M’busa Chipasi Chirwa ndiye wapereka langizoli mu ulaliki wake pa mpingo wa St Andrews CCAP munzinda wa Mzuzu.
“Kukhala membala wachipani chilichonse sikolakwika, mukhoza kukachita chi khristu ku chipani komweko posakalola kugwiritsidwa ntchito yochita ziwawa,” M’busa Chirwa anatero.
Iwo analangiza achinyamata kuti azindikire kuti andale amene amawatuma ndi akuluakulu kale komanso kwawo kwatsala kochepa.
Abusawa analangizanso akhristu kuti adzipereka msonkho ku boma moyenera monga momwe mawu a Mulungu amanenera kuti “perekani kwa Kaisara zake za Kaisara” m’bukhu la Maliko ndime 12 vesi ya 17.
M’busa Chirwa anati akhristu akuyenera kukhala okhulupirika ndi kuti kaya ali mumsika adzipereka msonkho wamumsikawo komanso ngati ali ndi ntchito zamalonda akuyenera kulipira moyenera
Olemba: Henry Haukeya