Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Azaumoyo akufufuza za imfa ya achinyamata aku Manase

Mu chinthuzi: Gift Kawalazira – Dotolo otsogolera ntchito zaumoyo ku Blantyre

Akuluakulu oona za umoyo munzinda wa Blantyre ati akufufuza za achinyamata ena amene malipoti akusonyeza kuti amwalira atamwa mowa wina  mdera la Manase mumzindawu.

Kalata imene yasayinidwa ndi dotolo otsogolera ntchito za zaumoyo ku Blantyre, a Gift Kawalazira, ikusonyeza kuti kafukufuku wa azachipatala wapeza kuti achinyamata asanu ndiwo amwalira pamene ena awiri akulandira thandizo pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth atamwa mowa umene akuuganizira kuti wadwalitsa anyamata awiriwo ndinso kupha asanu enawo.

Anthu ena ati achinyamata ambiri akumakonda kumwa mowawo mma shabeen, umene ndiwaukali ndipo ena akuutchula kuti ‘mbuye tengeni’.

 

Related posts

PRIVATE SECTOR URGED TO UTILISE OPPORTUNITIES

MBC Online

Government commits to youth development through digital initiatives

Rabson Kondowe

Malawians urged to bolster tourism

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.